
Olemba Lucky Milias
Atalepheraka kwa masabata angapo masewero olimbilana malo otsiliza mu mpikisano wa chikho cha ndalama zokwana 5 Million kwacha cha Aubrey Dimba, pakati pa Nyasa Big Bullets Reserve ndi Kamuzu Barracks Reserve masewerowa aliko kumapeto kwa sabata ino.
Mwina wake wa chikhochi Aubrey Dimba watsimikiza kuti timu ya Nyasa Big Bullets Reserve yomwe inali yotangwanika ndi masewero mchigawo cha ku mwera yatsimikiza kuti ikwanitsa kudzasewera masewerowa la mulungu pa bwalo la Aubrey Dimba ku Mchinji.
Malinga ndi Dimba wati akuembekezera masewero abwino pomwe matimuwa akufunitsitsa kuti afike mu ndime yotsiliza ndikudzakumana ndi timu ya Silver Strikers Reserve mu ndime yotsiliza ya mpikisanowu.
"Ndife okondwa kuti masewero omwe akhala akulepheleka masabata apitawa ulendo uno aliko ndipo tikuembekezera kuti timu ya bwino ndi yomwe idzapambane," Iye anatero.

Dimba waonjezera kuti mpikisanowu ukuembekezera kufika kumapeto kumayambiliro kwa mwezi December pomwe katswiri amene adzatenge ndalama zokwana za 1.5 Million adzadziwike.
Komabe iye anati kupatula masewero apakati pa matimuwa, akulu akulu oyendetsa masewerowa akozaso zinthu zina masewerowa asadayambe.
"Timaembekezera kumaliza mpikisanoku mwezi uno wa November koma chifukwa cha kusintha sintha kwa masiku omwe masewero a pakati pa Nyasa Big Bullets Reserve ndi Kamuzu Barracks Reserve ndi komwe kwangitsa kuti tifike mwezi wa mawa," Iye anatero.
Chaka chatha timu ya Nyasa Big Bullets Reserve ndi yomwe idali akatswiri a mpikisanowu pomwe idathambitsa timu ya Silver Strikers Reserve.
Pakadali pano timu ya Silver Strikers Reserve ndi yomwe idafika kale mu ndime yotsiliza ya mpikisanowu pomwe idagonjetsa timu ya Extreme kudzera pa ma penate masewrowa atathera kufanana mphamvu.
No comments:
Post a Comment