
Olemba Lucky Millias
Mphudzitsi wa timu ya Dedza Young Soccer Andrew Bunya wadandaula kwambiri ndi ndi oyimbira amene anaimbira masewero awo ndi timu ya Ekas Freight Wanderers mu mpikisano wa chikho cha Nyasa Capital Finance mchigawo chapakati.
Bunya wayankhula izi pomwe timu yake yagonja ndi chigoli chimodzi kwa chilowere pa khomo la Ekas Freight Wanderers pomwe chigoli chake anagoletsa ndi Mike Nkhata.
Koma poyankhula ndi Andrew Bunya wati oyimbira amene anaimbira masewero awo ndi munthu omvuta kumvetsa chifukwa ziganizo zake zinali zokondwera timu ya pakhomo.
"Kuimbira kwa nyasi ngati kumeneku ndi komwe kwapangitsa ife kuti tigonje ndipo ndikulephera kukumbukira tsiku lomwe kuimbira kwa mtundu ngati kumeneku ndidakuonako," Iye anadandaula motero.
Bunya anapitilizaso kupempha akulu akulu oyendetsa masewero a mpira wa miyendo mchigawo chapakati kuti akuyenera kukoza nkhani za kaimbilidwe ndipo kulephera apo mpira mchigawo chapakati umvuta kutukuka kwake.
"A Harawa ndi azizawo oyendetsa mpira mchigawo cha pakati ali ndi ntchito yaikulu kuti akoze mvuto limeneri koma kukamba za mpira ife a Dedza Young Soccer tasewera bwino kwambiri," Bunya anafotokoza motero.
Kumbali yake mphudzitsi wa timu ya Ekas Freight Wanderers Yassin Zinx wati amadziwa kuti apambana masewero amenewa chifukwa anakozekera bwino za masewerowa.
"Tinasewera bwino ndipo tinakozekera kuti tipambane masewerowa ndipo pano chidwi chathu ndikufuna kuchita bwino mu mpikisano umenewu," Anafotokoza motere Yassin.
Pakadali pano timu ya Ekas Freight Wanderers yafika mu ndime ya ma timu anai ndipo akhale akudziwa timu yomwe akumane nayo polimbirana malo a mu ndime yotsiliza ya mpikisanowu.
Ena mwa ma timu omwe afikakaso mu gulu la matimu anayi ndi Extreme, St Gabriel Medicals komaso Kawinga.
Chikho cha ndalama zokwana 8.5 Million chomwe kampani ya Nyasa Capital Finance ikuthandiza mchigawo chapakati chilibe omwe akuchiteteza kutsatira kutulaluka kwa timu yomwe idatenga chikhochi chaka chatha ya Silver Strikers Reserve ndi timu ya Zaithwa yomweso yatulutsudwa ndi timu ya St Gabriel Medicals kudzera pa ma penate masewero awo atathera kufanana mphamvu ndi chigoli chimodzi kwa chimodzi.
No comments:
Post a Comment