
Olemba Lucky Millias
Katswiri pa nkhani za masewero Willan Kamangoro Mkandawire wadzudzura ochemelera ena a timu ya Silver Strikers omwe akupitilizabe kuyankhula mawu a chipongwe kwa osewera wakale wa timuyi Maxwell Gasten Phodo pomwe katswiriyu wachoka ku timuyi.
Chilengezeleni akulu akulu a timuyi kuti Phodo saliso mbali imodzi ya Silver Strikers, ochemelera ena akhala akuyankhula mawu a chipongwe pa osewerayu kudzera pa masamba a mchezo monga Facebook komaso WhatsApp.
Malinga ndi zoyankhula za ochemelera ena ati Phodo wachita bwino kuchoka ku timuyi chifukwa analibe phindu pomwe chaka chino anakumana ndi namondwe wolephera kugoletsa zigoli ku timu yake yakaleyi.
Koma malinga ndi Mkandawire wati mu nthawi yomwe Phodo amatumikila timu ya Silver Strikers wakhala osewera amene waithandiza timuyi ndipo mkulakwa kwa kukulu kuti azilandira chitozo chotere.
"Pena pake ndi zomvuta kumvetsa kuti ochemelera ngati amenewa ayiwala kale zintchito za bwino zomwe Phodo wachita ku timu imenei.
"Wakhala akumwetsa zigoli zochuluka chaka chatha ndipo dzina lake lidali mkamwa mkamwa pomwe adagoletsa chigoli chofunikira pomwe timu yake idathambitsa timu ya Nyasa Big Bullets mu TNM Super League pa bwalo la Silver, tiziti zinthu ngati zimenezi ayiwala kale?" Iye anafusa.
Mkandawire anapitiliza kupempha ochemelera a ma timu dziko muno kuti asinthe pa kachitidwe kawo ka zinthu ndipo wati mkofunika kuti azilemekeza chiganizo cha osewera wina aliyese pamene wasankha kuchoka ndi kupita ku timu ina.
"Mvuto lonyoza osewera akachoka ku matimu omwe anali ndi kupita ku timu ina sikuti lili ku timu ya Silver Strikers kokha ai, izi ziliso chimodzi modzi kwa ochemelera a matimu ena dziko muno omwe ali ndi khalidwe ngati umenewu," Iye anatero.
Chaka chino Phodo wangokwanitsa kugoletsa chigoli chimodzi chokha pomwe anali ku timu ya Silver Strikers ndipo ngakhale timu ya Silver Strikers imafunabe kukhala ndi osewerayu amene mbuyomu adali osewera wa timu ya Mzuzu Warriors, Iye wasankha kuchoka ku timuyi pomwe gwirizano wawo udafika kumapeto.
Mbuyomu osewera ngati Precious Sambani, Jafali Chande, Enerst Kakhobwe, Chiukepo Msowoya, Miracle Gabeya, Henry Kabichi, Vitumbiko Kumwenda, Babatunde Adepoju komaso Muhammad Sulumba kungotchulapo ochepa adakumana nalopo mvuto ngati limeneli pomwe adasintha timu yomwe amatumikila ndi kupita ku matimu ena.
No comments:
Post a Comment